Isaiah 40:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo ali ngati mbeu zobzala posachedwa, kapena zofesa chatsopano, zongoyamba kumene kuzika mizu. Mbeuzo Chauta akaombetsa mphepo zimauma, ndipo mkuntho umaziwulutsa ngati mankhusu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene kapena kufesedwa chapompano, ndi kungoyamba kuzika mizu kumene ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kabvumvulu awacotsa monga ciputu.