Isaiah 40:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani. Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi? Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo, nayitana iliyonse ndi dzina lake. Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri, palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene aturutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azicha zonse maina ao, ndi mphamvu zace zazikuru, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.