Isaiah 40:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga kuma osalema; adzayenda koma osalefuka.