Isaiah 40:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudamveka mau akuti, “Lengeza.” Ine ndidafunsa kuti, “Kodi ndilengeze chiyani?” Mau aja adati, “Ulengeze kuti anthu onse ali ngati udzu. Kukongola kwao kuli ngati maluŵa akuthengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wina ananena kuti, “Lengeza.” Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani? “Pakuti anthu onse ali ngati udzu ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau a wina ati, Pfuula. Ndipo ndinati, Kodi ndipfuule ciani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;