Isaiah 40:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwera pa phiri lalitali, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Yerusalemu. Ufuule kwamphamvu, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Ziyoni. Kweza mau, usaope. Uuze mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba pa phiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumidzi ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni, kwera pa phiri lalitali. Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu, fuwula kwambiri, kweza mawu, usachite mantha; uza mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba pa phiri lalitari; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena ku midzi ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!