Isaiah 41:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu akuti, “Mukhale chete ndipo mundimvere, inu maiko a m'mphepete mwa nyanja. Anthu a mitundu yonse akhale ndi mphamvu zatsopano. Asendere ndi kulankhulapo. Tiyeni tikhale pamodzi pa mlandu atiweruze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khalani chete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni tiyandikire pamodzi kuchiweruziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja! Alekeni ayandikire ndi kuyankhula; tiyeni tikhale pamodzi kuti atiweruze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khalani cete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni, tiyandikire pamodzi kuciweruziro.