Isaiah 41:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usaope, iwe Yakobe, wofooka ngati nyongolotsi, usachite mantha, iwe Israele, wooneka ngati mtembo, chifukwa Ineyo ndidzakuthandiza. Mpulumutsi wako ndine, Woyera uja wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi, iwe wochepa mphamvu Israeli, chifukwa Ine ndidzakuthandiza,” akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israyeli; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israyeli.