Isaiah 41:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu, chatsopano, cha mano akuthwa. Udzanyenya mapiri ndi kuŵaphwanyaphwanya. Magomo udzaŵasandutsa mankhusu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri. Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya, ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ndidzakuyesa iwe coombera tirigu catsopano cakuthwa cokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.