Isaiah 41:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzaŵapeta, ndipo adzauluka ndi mphepo nadzamwazika ndi namondwe. Koma iwe udzakondwa chifukwa choti Ine ndine Mulungu wako. Udzapeza ulemerero chifukwa cha Ine, Woyera uja wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso adzamwazika ndi kamvuluvulu. Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako, ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe udzawakupa, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kabvumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israyeli,