Isaiah 41:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi ndani adabweretsa wogonjetsa uja wochokera kuvuma, wonka napambana kulikonse kumene amapita? Ndani amamthandiza kuti apambane anthu a mitundu ina, ndi kugonjetsa mafumu? Lupanga lake limaŵasandutsa anthuwo kukhala ngati fumbi lapansi, uta wake umaŵamwaza ngati mankhusu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndani anadzutsa wochokera kummawa uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita? Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani anautsa wina wocokera kum'mawa, amene amuitana m'cilungamo, afike pa phazi lace? Iye apereka amitundu patsogolo pace, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga pfumbi ku lupanga lace, monga ciputu couluzidwa ku uta wace.