Isaiah 41:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu adzaona ndi kudziŵa, adzazindikira ndi kumvetsa kuti Chauta ndiye adachita zimenezi, kuti Woyera uja wa Israele ndiye adakonza zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lachita ichi, ndipo Woyera wa Israele wachilenga ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti anthu aone ndi kudziwa; inde, alingalire ndi kumvetsa, kuti Yehova ndiye wachita zimenezi; kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lacita ici, ndipo Woyera wa Israyeli wacilenga ici.