Isaiah 41:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiwuzenitu zimene zidzachitike kutsogolo kuti tidziŵe kuti ndinu milungudi. Chitani zabwino kapena kubweretsa masoka, kuti mutidabwitse ndi kutichititsa mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tchulani zinthu zimene zilinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, chitani zabwino, kapena chitani zoipa, kuti ife tiopsedwe, ndi kuona pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani, ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu. Chitani chinthu chabwino kapena choyipa, ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Chulani zinthu zimene zirinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, citani zabwino, kapena citani zoipa, kuti ife tiopsyedwe, ndi kuona pamodzi.