Isaiah 41:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndautsa munthu wina kumpoto, ndipo wabwera. Munthuyo, kuchokera chakuvuma, amamva kuitana pomutchula dzina. Amaponda olamulira ngati matope, monga m'mene munthu woumba mbiya amapondera mtapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera, munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana. Amapondaponda olamulira ngati matope, ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndautsa wina wakucokera kumpoto; ndipo iye wafika wakucokera poturuka dzuwa, amene achula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.