Isaiah 41:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani adaululiratu zimenezi poyamba pomwe kuti ife tidziŵe? Ndani adatiwuziratu zimenezi zisanachitike, kuti ife tinene kuti, ‘Wakhoza?’ Palibe ndi mmodzi yemwe adazinena, palibe ndi mmodzi yemwe adazilengeza, ndipo palibe amene adamva mau anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani watchula icho chiyambire, kuti ife tichidziwe? Ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? Inde, palibe wina amene atchula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde palibe wina amene amvetsa mau anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe, kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’ Palibe amene ananena, palibe analengeza zimenezi, palibe anamva mawu anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani wachula ico ciyambire, kuti ife ticidziwe? ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? inde, palibe wina amene achula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde, palibe wina amene amvetsa mau anu.