Isaiah 41:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a maiko a m'mphepete mwa nyanja aona zimene ndachita ndipo aopsedwa, anthu a pa mathero a dziko lapansi ali njenjenje. Akusendera pafupi, akubwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa; anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera. Akuyandikira pafupi, akubwera;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.