Isaiah 41:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakutenga kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndidakuitana kuchokera ku mbali zakutali za dziko. Ndipo ndidzakuuza kuti, “Iwe ndiwe mtumiki wanga, ndidakusankhula, sindidakutaye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kuchokera m'ngodya zake, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi. Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’ Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kucokera m'ngondya zace, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;