Isaiah 42:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye. Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza, amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye. Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzaturutsira amitundu ciweruziro.