Isaiah 42:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu akuti, “Ndakhala ndili chete pa nthaŵi yaitali, ndidangoti phee, osachita kanthu. Koma tsopano ndikubuula ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira, ndikupuma modukiza ndipo ndili ŵefuŵefu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali, ndakhala ndili phee osachita kanthu. Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira, ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula; ndakhala cete ndi kudzithungata ndekha; tsopano ndidzapfuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.