Isaiah 42:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatsogolera anthu akhungu m'miseu imene sadaidziŵe, ndidzaŵaperekeza pa njira zimene sadadzerepo konse. Ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwao kuti ukhale kuŵala, ndipo ndidzasalaza malo osasalala. Zimenezi ndidzazichitadi ndipo sindidzazilekera padera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe, ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo; ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala ndipo ndidzasalaza malo osalala. Zimenezi ndizo ndidzachite; sindidzawataya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa; m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu Izi ine ndidzacita, ndipo sindidzawasiya.