Isaiah 42:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsono anthu ameneŵa aŵalanda ndi kuŵafunkhira zinthu zao. Onseŵa adaŵakola m'mbuna, ndi kuŵabisa m'ndende. Adaŵafunkhira, popanda wina woŵapulumutsa, adaŵabera, popanda wina wonena kuti, “Bwezani!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo, onsewa anawakola mʼmaenje kapena akuwabisa mʼndende. Tsono asanduka chofunkha popanda wina wowapulumutsa kapena kunena kuti, “Abwezeni kwawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba zakaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.