Isaiah 42:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani adapereka Yakobe kwa ofunkha? Ndani adapereka Israele kwa anthu akuba? Kodi akuchita zimenezi si Chauta? Paja tidamchimwira, sitidatsate njira zake, ndipo sitidamvere malamulo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israele, kuti awawanyidwe? Kodi si Yehova? Iye amene tamchimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zake, ngakhale kumvera chiphunzitso chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha, ndi Israeli kwa anthu akuba? Kodi si Yehova, amene ife tamuchimwirayu? Pakuti sanathe kutsatira njira zake; ndipo sanamvere malangizo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israyeli, kuti awawanyidwe? kodi si Yehova? Iye amene tamcimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zace, ngakhale kumvera ciphunzitso cace.