Isaiah 42:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadzafookera kapena kutaya mtima, mpaka atakhazikitsa chilungamocho pa dziko lapansi. Maiko akutali akuyembekeza malamulo ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
sadzafowoka kapena kukhumudwa mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi, ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa ciweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira cilamulo cace.