Isaiah 42:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu, Chauta, adalenga zakuthambo ndi kuziyalika. Adalenga dziko lapansi ndi zonse zimene limabereka. Adapatsa mpweya kwa anthu okhala m'dzikomo, ndi kuninkha moyo kwa onse oyendamo. Iyeyo akunena kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika, amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka, amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo, ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi cimene cituruka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;