Isaiah 42:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta ndakuitana kuti ukhazikitse chilungamo. Ndakugwira padzanja ndi kukusunga. Ndakusankhula kuti ukhale chipangano kwa anthu, ukhale kuŵala kounikira anthu a mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine Yehova ndakuitana Iwe m'chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama; ndikugwira dzanja ndipo ndidzakuteteza. Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine Yehova ndakuitana Iwe m'cilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;