Isaiah 42:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzaŵatsekula maso anthu akhungu, udzamasula akaidi m'ndende, udzatulutsa m'ndende anthu okhala mu mdima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzatsekula maso a anthu osaona, udzamasula anthu a mʼndende ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti utsegule maso akhungu, uturutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, aturuke m'nyumba ya kaidi.