Isaiah 43:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano, Yehova amene anakulenga, iwe Yakobo, amene anakuwumba, iwe Israeli akuti, “Usaope, pakuti ndakuwombola; Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, cifukwa ndakuombola iwe, ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga.