Isaiah 43:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa; ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu. Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wacilendo pakati pa inu; cifukwa cace inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.