Isaiah 43:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo, gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu, ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene aturutsa gareta ndi ka valo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.