Isaiah 43:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano! Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona? Ine ndikulambula msewu mʼchipululu ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ine ndidzacita cinthu catsopano; tsopano cidzaoneka; kodi simudzacidziwa? Ndidzakonzadi njira m'cipululu, ndi mitsinje m'zidalala.