Isaiah 43:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi zinandilemekeza. Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyama za m'thengo zidzandilemekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; cifukwa ndipatsa madzi m'cipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;