Isaiah 43:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simudandigulire bango lonunkhira, simudandipatse mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma m'malo mwake inu mwanditopetsa ndi machimo anu, mwandilemetsa ndi zolakwa zanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndalama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi machimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simunandigulire bango lonunkhira kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndarama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi macimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.