Isaiah 43:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero, ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndidzaipitsa akuru a kacisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israyeli akhale citonzo.