Isaiah 43:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu Ine ndine Chauta, Mulungu wako. Ndine Woyera uja wa Israele, Mpulumutsi wako. Ndidzapereka Ejipito pofuna kuwombola iwe. Ndidzapereka Etiopiya ndi Seba m'malo mwa iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako, Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako. Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe, ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israyeli, Mpulumutsi wako; ndapatsa Aigupto dombolo lako, Etiopia ndi Seba m'malo mwako.