Isaiah 43:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga, ndipo chifukwa ndimakukonda, ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokhala iwe wa mtengo wapatari pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.