Isaiah 43:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzauza akumpoto kuti ‘Muŵaleke.’ Ndidzalamula akumwera kuti ‘Musaŵagwire.’ Ana anga aamuna abwerere kuchokera ku maiko akutali, ana anga aakazi abwerere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kuchokera kutali, ndi ana anga akazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kucokera kutari, ndi ana anga akazi kucokera ku malekezero a dziko lapansi;