Isaiah 43:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitundu yonse ya anthu isonkhane, anthu a m'maiko onse akhalepo pamlandupo. Ndani mwa iwo adaathapo kuneneratu zimenezi? Ndani mwa iwo adaathapo kutifotokozera zakale? Abwere ndi mboni zao, kuti zidzatsimikize mau ao, kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, ‘Nzoonadi.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? Atenge mboni zao, kuti avomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi, anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu. Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi? Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale? Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona, kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ici ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.