Isaiah 44:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo nachiika pa moto. Ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pakuchimenya ndi nyundo. Pambuyo pake amamva njala natha mphamvu, akapanda kumwa madzi, amalefuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo ndipo amachiyika pa makala amoto; ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pochimenya ndi nyundo. Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu; iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wacipala acita zace ndi nsompho, nagwira nchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira nchito yace ndi mkono wace wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zace zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.