Isaiah 44:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmisiri wa matabwa amayesa mtengo ndi chingwe. Amalembapo chithunzi ndi cholembera, nachizokota ndi zipangizo zake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola, kuti achiike m'nyumba ya chipembedzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mmisiri wa mitengo atambalitsa chingwe; nalilemba ndi cholembera, nalikonza ndi ncherero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera; amasema bwinobwino ndi chipangizo chake ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mmisiri wa mitengo atambalitsa cingwe; nalilemba ndi colembera, nalikonza ndi ncerero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba.