Isaiah 44:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amagwetsa mitengo ya mkungudza. Mwinanso amasankhula mtengo wa paini kapena wa thundu ku nkhalango. Mwina mwake amabzala mtundu wina wa paini ndipo umakula ndi mvula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amagwetsa mitengo ya mkungudza, mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango, ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.