Isaiah 44:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigawo china amasonkhera moto wootchapo nyama imene amadya mpaka kukhuta. Amaothanso motowo namanena kuti, “Aha! Ndikumva kufunda! Ati kukoma motowu ati!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye atenthako mbali ina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto wowotcherapo nyama imene amadya, nakhuta. Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti, “Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye atenthako mbali yina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga, nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto.