Isaiah 44:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi chigawo chotsala amapanga kamulungu kake, fano lake limenelo. Amaliŵeramira ndi kumalipembedza. Amapemphera kwa fanolo namanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, undipulumutse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chotsalacho apanga mulungu, ngakhale fano lake losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, chifukwa kuti ndinu mulungu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo; amaligwadira ndi kulipembedza. Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cotsalaco apanga mlungu, ngakhale fano lace losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, cifukwa kuti ndinu mulungu wanga.