Isaiah 44:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu otere sadziŵa kanthu ndipo samvetsa konse. Maso ao ndi omatirira, sangathe kupenya. Nzeru zaonso nzogontha, sangathe kumvetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse; maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona, ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, cifukwa pamaso pao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwao kuti sangadziwitse.