Isaiah 44:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndine Chauta amene ndidakulengani ndi kukuumbani m'mimba mwa amai anu, amenenso ndinkakuthandizani. Usaope iwe Yakobe, mtumiki wanga. Inu ndinu anthu anga okondedwa amene ndidakusankhulani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kuchokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako, ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti, Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga, Yesuruni, amene ndinakusankha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kucokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.