Isaiah 44:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo akuchita ngati kudya phulusa, maganizo ake opusa amsokeretsa kotero kuti sangapulumutsenso moyo wake. Sangathenso kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili m'manja mwangachi si chabodza?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa; motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wace, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?