Isaiah 44:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Ukumbukire zimenezi, iwe Yakobe, popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israele. Ndidakulenga, ndiwe mtumiki wanga. Iwe Israele sindidzakuiwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumbukirani zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli. Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga; iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumbukira zinthu izi, Yakobo; ndi Israyeli, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israyeli, sindidzakuiwala.