Isaiah 44:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo, ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa. Bwerera kwa Ine, popeza ndakupulumutsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndafafaniza monga mtambo wocindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo macimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.