Isaiah 44:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga, pakuti Chauta wagwiradi ntchito. Fuula iwe dziko lapansi. Yambani nyimbo, inu mapiri, ndiponso inu nkhalango ndi mitengo yanu yonse, chifukwa Chauta waombola Yakobe, waonetsa ulemerero wake mwa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi pa dziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi; fuwula, iwe dziko lapansi. Imbani nyimbo, inu mapiri, inu nkhalango ndi mitengo yonse, chifukwa Yehova wawombola Yakobo, waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yimbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wacicita ico; kuwani inu, mbali za pansi pa dziko; yimbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; cifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israyeli.