Isaiah 44:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndine amene ndimalepheretsa mipingu ya anthu onama, ndi kupusitsa anthu oombeza ula. Ndine amene ndimatsutsa mau a anthu anzeru, ndi kuŵaonetsa kuti nzeru zao nzopusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga, ndipo ndimapusitsa owombeza mawula. Ndimasokoneza anthu a nzeru, ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndine amene nditsutsa zizindikilo za matukutuku, ndi kucititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao: