Isaiah 44:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndine amene ndimatsimikiza mau a mtumiki wanga, ndi kupherezetsa zimene amithenga anga adaneneratu. Ndine amene ndimanena za Yerusalemu kuti anthu adzakhalanso kumeneko, ndi kunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti idzamangidwanso. Ine ndidzautsanso malo ao amene adagwetsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za midzi ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake. “Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu. Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso. Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kucita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za midzi ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ace.