Isaiah 44:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina adzanena kuti ‘Ine ndine wa Chauta,’ wina adzadzitchula wa m'banja la Yakobe. Winanso adzalemba padzanja pake kuti, ‘Wa Chauta,’ ndipo adzadzitchula wa m'banja la Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’ wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo; winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wina adzati, Ine ndiri wa Yehova; ndi wina adzadzicha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lace, Ndine wa Yehova, ndi kudzicha yekha ndi mfunda wa lsrayeli.